Isaiah 56

Chipulumutso kwa Anthu Ena Onse

1Yehova akuti,

“Chitani chilungamo
ndi zinthu zabwino,
chifukwa chipulumutso changa chili pafupi
ndipo ndidzakuwombolani posachedwapa.
2Ndi wodala munthu amene amachita zimenezi,
munthu amene amalimbika kuzichita,
amene amasunga Sabata osaliyipitsa,
ndipo amadziletsa kuchita zoyipa.”

3Mlendo amene waphatikana ndi Yehova asanene kuti,
“Ndithu Yehova wandichotsa pakati pa anthu ake.”
Ndipo munthu wofulidwa asanene kuti,
“Ine ndine mtengo wowuma basi.”
4Popeza Yehova akuti,

“Wofulidwa amene amasunga masabata anga,
nachita zokomera Ine
ndi kusunga pangano langa,
5ndidzawapatsa dzina ndi mbiri yabwino
mʼkati mwa Nyumba yanga ndi makoma ake,
kuposa kukhala ndi ana aamuna ndi aakazi.
Ndidzawapatsa dzina labwino,
losatha ndi losayiwalika.”
6Yehova akuti, “Alendo amene amadziphatika kwa Yehova,
motero kuti amamutumikira Iye,
amakonda dzina la Yehova,
amamugwirira ntchito,
komanso kusunga Sabata osaliyipitsa
ndi kusunga bwino pangano langa,
7amenewa Ine ndidzawafikitsa ku phiri langa lopatulika,
ndidzawapatsa chimwemwe mʼnyumba yanga ya mapemphero.
Zopereka zawo zopsereza ndi nsembe zawo
ndidzazilandira pa guwa langa la nsembe.
Paja nyumba yanga idzatchedwa
nyumba ya mapemphero ya anthu a mitundu yonse.”
8Ambuye Yehova, amene amasonkhanitsa
Aisraeli onse ali ku ukapolo akunena kuti,
“Ndidzasonkhanitsano anthu ena
kuwonjezera amene anasonkhana kale.”

Mulungu Adzazula Anthu Oyipa

9Bwerani, inu zirombo zonse zakuthengo,
inu nonse zirombo zamʼnkhalango bwerani mudzadye!
10Atsogoleri onse a Israeli ndi akhungu,
onse ndi opanda nzeru;
onse ndi agalu opanda mawu,
samatha kuwuwa:
amagona pansi nʼkumalota
amakonda kugona tulo.
11Ali ngati agalu amene ali ndi njala yayikulu;
sakhuta konse.
Abusa nawonso samvetsa zinthu;
onse amachita monga akufunira,
aliyense amafunafuna zomupindulitsa iye mwini.
12Aliyense amafuwulira mnzake kuti, “Bwera, tiye timwe vinyo!
Tiyeni timwe mowa mpaka kukhuta!
Mawa lidzakhala ngati leroli,
kapena kuposa lero lino.”
Copyright information for NyaCCL